Bungwe Loyang’anira ulimi ndi ulimi a fodya m’Malawi la Tobacco Commission (TC) likukumbutsa alimi a fodya ndi mabungwe a alimi a fodya kuti kalembera wa alimi a fodya ali mkati ku ma ofesi a bungweli komanso malo ena aku midzi. Alimi omwe akonzeka kulima fodya chaka cha mawa akudziwitsidwa kuti tsiku lotseka kalemberayu ndi pa 30th September 2020.

Bungweli likudziwitsanso alimi a fodya kuti kulima ndi kugulitsa fodya wopanda chiphaso/chilorezo nkosaloledwa ndipo ndi mlandu. Kukonzekera kwa ulimi wa fodya kumayamba ndi kalembera. Alimi akuyenera kuti alembetsa asanapitilire ndi ndondomeko zina zolima fodya.

Alimi akuyenera kulima fodya molingana ndi mlingo womwe mwapatsidwa ndi bungwe la Tobacco Commission pa nthawi ya kalembera. Choncho, alimi onse omwe akonzeka kulima fodya chaka cha mawa koma sanalembetse apite ku ma ofesi a bungweli kuti akalembetse.

Kumbukirani kuti nthenda ya COVID-19 iripo, choncho tenganipo mbali podziteteza komanso kuteteza ena posamba m’manja pafupipafupi ndi sopo komanso povala zophimba pakamwa ndi pamphuno (face masks).

Bungweli likufunira alimi onse a fodya chaka chopambana cha 2020/2020.